Kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya dziko lino, Bank ya FDH ikhala ikukhazikitsa ndondomeko yogwiritsa ntchito mfundo za chisilamu posunga ndi kubwereketsa ndalama ija pa chingerezi amati Islamic Banking.
Mwambowu omwe anthu ndi mabungwe osiyana siyana akhala akuuyembekezera, uchitika chakumasanaku munzinda wa Blantyre.