MAM Yapempha Asilamu Akatsegule Account Ndi FDH Islamic Banking

Wapambando wa bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM) Sheikh Idrisa Muhammad akuti chilengezereni a FDH Bank masiku atatu apitawa, kuti akhazikitsa Islamic Banking mdziko muno, iwo ngati bungwe la MAM akulandira pempho kuchokera ku ma bank ena mdziko muno kuti nawo ayambise Islamic Banking.

Iwo ati izi ndi zomwe amayembekezera, ndipo akufunisitsa ikamafika miyezi inayi asilamu ochuluka akhale ayamba kusungisa ndalama zawo ku FDH Salama Banking Solution.

Mtsogoleriyu wapempha asilamu onse mdziko muno kuti akatsegulise mwansangansanga ma account awo ndi FDH SALAMA BANKING SOLUTION.

Sheikh Idrisa Muhammad ayankhula izi mmawa wa lero ku Mudi ku Limbe ku ma ofesi a Darusunnah Foundation komwe bungwe la Darusunnah Foundation lakhala bungwe loyambilira kutsegulira ma account ku FDH Salama Banking Solution kwa ana amasiye omwe bungweli limawathandiza.

Ndalama zokwana 35 miliyoni kwacha ndi zomwe bungwe la Darusunnah Foundation layika ku FDH Salama Banking Solution ndipo ana amasiye okwanira 74 ochokera mmaboma osiyanasiyana mdziko muno ndi omwe alandira ndalamazi.

Abdul Rahman Chowe yemwe ali Mlembi wankulu wa Darusunnah Foundation wati bungweli lafuna kukhala lachitsanzo chabwino popereka sapoti ku FDH Salama Banking Solution ndi cholinga mabungwe ena achisilamu nawonso atatero.

Related Posts

Malawi Freedom Network advice President Banda to fight corruption

If you thought Malawians are lazy people, I bet you a Dinosaur, think twice and you will know, check in Read more

David Bisnowaty Israeli-Born Malawi Parliament Member: Actions, Not Words, Will Change Africa for the Better

Malawi MP David Bisnowaty. How does the Israeli-born son of an eastern European Holocaust survivor end up as a parliament Read more

Biography Of Zuneth Sattar

Zuneth Sattar Director of Xaviar Limited and Xaviar Investments Limited Zuneth Sattar is an experienced and knowledgeable property investor. With Read more

Zuneth Sattar Is An Experienced Property Investor

PROPERTY INVESTOR PROPERTY MARKET AN OVERVIEW This blog will cover a wide range of topics and subjects that relate to Sattar’s Read more

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window