Tuesday, April 16
Shadow

Mpinganjira Mlendo Womelekezeka Pamgonelo Womwe Linakonza Bungwe La SULOM

Mmodzi mwa anthu akuluakulu ochita malonda mdziko muno Dr Thomson Mpinganjira waulura kuti chaka chatha ankafuna kusiya kuthandiza timu ya Mighty Mukuru Wanderers kamba ka kaimbiridwe koipa komanso khalidwe lowononga zinthu la ochemelera ena.

Mpinganjira anali mlendo womelekezeka pamgonelo womwe linakonza ndibungwe la SULOM loweluka munzinda wa Lilongwe.

Chaka chatha ochemelera ena a Wanderers anaphwanya mipando pa bwalo la Bingu posagwirizana ndi ziganizo za woimbira Godfrey Nkhakananga pamasewero amu Airtel Top 8 pakati pa iwo ndi Silver Strikers.

Poyankhula ndi MIJ FM Mpinganjira wati akufuna mabungwe a SULOM ndi FAM kuti akonze zinthu monga kaimbiridwe koipa komwe kamakwiyitsa otsatira timuyi ponena kuti izi ndizina mwa zinthu zomwe zikubwezeretsa mmbuyo masewero ampira wamiyendo.

Mpinganjira anawonjezera kudzudzula khalidwe la ochemelera ena lowononga zinthu ponena kuti chaka chatha amafuna kusiya kuthandiza mpira koma anaganiza kuti pamapeto nditimu ya Noma ndi osewera omwe angavutike kwambiri.

Umu ndimomwe Mpinganjira anayankhulira chingelezi ndi Chichewa kwa wolemba nkhan munzinda wa Lilongwe i

See also  Mighty Mukuru Wanderers yet to release players for Flames camp

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

President Lazarus Chakwera has officially opened the Blantyre International Cancer Centre, The private health facility, has been constructed by the Thomson and Barbara Mpinganjira Foundation