Kutsatira mvula yochuluka imene inadza kamba ka Namondwe wa Freddy, nyanja ya Chilwa ku Zomba yadzadza pomwe madzi tsopano afika midzi yoyandikana ndi nyanjayi.
Malingana ndi a Fanuel Sadik, amene amakhala kuderali, madzi afika midzi yoyandikila doko la Kachulu komanso Mchenga ndipo anthu asamukira madera ena.
Khansala waderali, a Douglas January, anatsimikiza izi ndipo anati pakali pano kufika kunyanjaku pagalimoto ndikosatheka.
Zithuzi zikuonetsa momwe zinthu ziliri ku nyanjayi.