Wednesday, February 28
Shadow

Mgwilizano Wa Tonse Walephera Kukwanilisa Malonjezo

Akatswiri adzudzula boma la mgwirizano wa Tonse ati kamba kosakwaniritsa ena mwa malonjeza omwe unapereka kwa a Malawi usanalowe m’boma.

Izi zikubwera pomwe patha zaka zitatu dziko lino litachititsa chisankho chamtsogoleri chachibweleza pa 23 June mchaka cha 2020.

Moses Mkandawire, Wapampando wa bungwe la National Anti-Corruption Alliance, wati pakhala pali nkhani zakatangale zokhudza akuluakulu ena aboma.

Mkandawire wati izi ndi chifukwa choti bomali silikuikila chidwi chenicheni chithana ndi mchitidwe wa katangale.

Mkuikilapo ndemanga yake George Phiri katswiri pa nkhani za ndale wati kulephela kwa boma la mgwilizano wa Tonse kukwanilitsa zomwe linalonjeza kukukwiitsa amalawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *