Wednesday, February 28
Shadow

Apolisi Adzudzula Mchitidwe Wa Ziwawa

Wolemba: Rachael Julaye–LILONGWE

Apolisi ku Lilongwe adzudzula mchitidwe wa anthu ena a mmudzi mwa Funsani T/A Masula omwe Loweruka awotcha komanso kuononga katundu wa munthu wina ochita malonda pomuganizira kuti wapha m’bale wawo.

Mneneri wa polisiyi, Hastings Chigalu wati Lachinayi masana munthuyo anagwidwa akuba mu shop ya a Gilbert Faniwel ndipo anthu adamumenya modetsa nkhawa.

Chigalu wapitirila kufotokoza kuti munthuyo anamwalira patangodutsa tsiku limodzi kamba kovulalirla mkati ndipo akuti Loweruka mwambo wa maliro utangotha anthuwa anayamba kuononga katundu wa Faniwel.

“Wina mwa katundu yemwe anawonongedwa ndi monga nyumba, grocery komanso chimanga chosatong’ola chomwe ndi chandalama zochuluka,” watero Chigalu.

Iye wati apolisi anathamangira ku maloko komwe anadzetsa bata ndipo akhazikitsa kafukufuku ofuna kupeza onse omwe achita ziwawazi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *