Civil Service United ndi MAFCO FC alepherana posagoletsana

Ma timu a Civil Service United ndi MAFCO FC alepherana posagoletsana chigoli chili chonse ngati zopangana pamasewero omwe analipo masanawa pa bwalo la Civo mu ligi ya TNM.

Poyankhula atatha masewerowa, wachiwiri kwa mphunzitsi ku Civil, Wilson Chidati, wamvomereza kuti mpira unawavuta kamba koti chili chonse chomwe anakonzekera sichinatheke pamasewerowa.

Kumbali yake, wachiwiri kwa mphunzitsi ku timu ya Mafco, Jimmy Mzunga, wati anabwera ngakhale abwera kuti adzapambene, komabe walimbikitsa osewera ake kuti masewero otsatira adzachite bwino.

Timu ya Civil yafika pa nambala 5 itasewera masewero 20 ndipo ili ndi mapointi 28 pamene Mafco ili pa nambala 8 pamasewero 20 ndipo ali ndi 27.

Christopher Gototo ndi yemwe anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa osewera onse pamasewerowa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *