ndani adanamiza Chakwera kuti ndege yomwe Idaphetsa A Chilima ndi ena 8 idafika ku Mzuzu?

download

Bungwe la CDEDI lati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akuyenera kubwera poyera ndi kuyankhulapo pa zomwe adayankhula itachitika kumene ngozi ya ndege yomwe idachitika ku nkhalango ya Chikangawa.

Mkulu wa bungweli Sylvester Namiwa wayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe.

Iwo ati ambiri ndi mboni mdziko muno kuti Dr Chakwera adauza anthu kuti ndege yomwe adakwera Dr Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu idafika ku Mzuzu ndipo adauzidwa kuti abwelere.

Koma malingana ndi lipoti lomwe latuluka lachisanu lapitali lapeza kuti ndegeyi sidafika ku Mzuzu.

Bungweli lati a Malawi ndi odabwa kuti asilikali adaletsa anthu kufika ku malo angoziyi, ndi ndani yemwe adakankha phapha la ndegeyi kuchoka pa malo omwe idagwera kukafika mbali ina?

A Namiwa ati ngakhale bungwe lawo lilibe ukadaulo wotanthauzira lipotili, koma muli zambiri zotsutsana ndi zomwe Dr Chakwera adauza mtundu wa aMalawi.

kotero a Namiwa ati a Chakwera abwere poyera nkuulura kuti ankawapatsa uthenga omwe ankapereka kwa a Malawi ndi ndani ndipo cholinga chake chidali chani ponamiza mtundu wa a Malawi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *