Ndimulankhule Chakwera–Mutharika

Mtsogoleri wa chipani cha DPP Peter Mutharika wati ali ndi mau omwe akufuna kumuuza mtsogoleri wa dziko lino yemweso ndi mtsogoleri wa chipani cha MCP Lazarus Chakwera lachitatu likudzali.

Mutharika wayankhula izi kudzera kwa mneneri wake Shadrick Namalomba.

Poyankhula ndi MIJ Online Namalomba wati Mutharika ali ndi mau omwe akufuna kuuza Chakwera pa za kuvulazidwa kwa anthu otsatira DPP mu mzinda wa Lilongwe.

“Ngakhale a Mutharika akhale akuyankhula ku mtundu wa a Malawi Lachitatu lino pa ziwawa-zi koma kweni kweni uthenga-wu udzakhala ukupita kwa a Chakwera, ” watero Namalomba.

Namalomba wauza MIJ Online kuti ali ndi umboni ochuluka kuti chipani cha MCP ndi chomwe chavulaza otsatira DPP kaamba ka number plate ya galimoto yomwe inanyamula anthu-wo akuti mwini wake ndi wa MCP.

Padakali pano chipani cha MCP chakana kuti sichikukhudzidwa pa zipolowezi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *