Chipani Cha DPP Agwirizana Kuti Nankhumwa akhalebe pampandowu.
Kusamvana komwe kunalipo m’chipani cha DPP pa yemwe akuyenera kukhala mkulu wa zipani zotsuta boma m’nyumba ya malamulo kwatha tsopano. Izi zikutsatira m’gwirizano omwe mbali zokhuzidwa zapanga kuti a Kondwani Nankhumwa akhalebe pampandowu. Malingana ndi mneneri wa chipani cha DPP, Shadrec Namalomba, a Nankhumwa akhalabe pa udindowu kufikira pomwe chipanichi chidzachititsenso chisankho china cha mtsogoleri […]
