Dedza Dynamos FC tsopano izitchedwa Premier Bet Dedza Dynamos FC

Timu ya Dedza Dynamos FC tsopano izitchedwa Premier Bet Dedza Dynamos FC kutsatira thandizo la ndalama zokwana K100 million zomwe kampaniyi yapereka lero.

Mgwirizanowu ndi wa chaka chimodzi ndipo mkulu wa Premier Bet, a Trevor Whitaker wati akuyembekezera zotsatira zabwino ku timuyi mu ligi ya TNM.

Mmawu ake, mkulu wa timuyi a Hastings Mpanbira wati apweteka matimu chaka chino.

Naye mtsogoleri wa Football Association of Malawi {Fam} a Fleetwood Haiya wayamikira kampani ya Premier Bet kamba ka thandizoli pomwe wati izi zibweretsa mangolomera ku timuyi komanso kampani zina.

Premier Bet iziperekanso ndalama zokwana 100 thousand kwacha kwacha kwa wosewera mmodzi wapamwamba mwezi uli onse, 500 thousand kwacha kwa osewera mbambande pamapeto a ligi komanso 200 thousand kwacha kwa ochemelera wapamwamba ku timuyi.

Related Posts

Malawi Freedom Network advice President Banda to fight corruption

If you thought Malawians are lazy people, I bet you a Dinosaur, think twice and you will know, check in Read more

Mustag Chothia, Sulema Ismael Karim In Land scam

Land remains one area that Malawians know has been heavily abused, characterised by ownership wrangles, not to mention corruption, fueled Read more

The Concerned Citizens Furious With Chizuma’s Stubbornness

The concerned citizens group which is advocating for sanity in civil service have vowed to take drastic measures in responding Read more

Zuneth Sattar Speaks Out- I’m Not Shaken, It’s Just Mere Social Media Speculations

Public is being fed with social media lies propagated by some misguided individuals over personal vendetta. The move is just Read more

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window