FDH Salama Banking solutions yakhazikitsidwa tsopano ndi Bank ya FDH

Ndondomeko yobwereketsa ndi kusunga ndalama mogwirizana ndi malamulo achisilamu yomwe ikutchedwa FDH salama Banking solutions yakhazikitsidwa tsopano ndi Bank ya FDH.

Malingana ndi wa pa mpando oyendetsa bank ya FDH, charity Mseka, ntchitoyi iyambira mu nthambi zake za Limbe, city center ku Lilongwe komanso Mangochi.

Mseka wati ndondomekoyi ikupeleka mwayi kwa anthu omwe akhala akusakasaka kutukula ntchito zawo za chuma koma amalephera kupeza mwayi otere kwa nthawi yaitali.

Mseka wati ndondomekoyi imalimbikitsa kuchita zinthu moonekera, mokomera aliyense komanso kuthandizana panthawi yomwe zinthu zavuta.

Iye wati iyi ndi ndondomeko yokhayo yopilira pa nthawi yomwe chuma chikuvuta kaamba koti imalimbikitsa kukhala ndi katundu.

Mmawu ake, wapampando wakomiti yopereka ulangizi pa nkhani za malamulo achisilamu sheikh Ibrahim Lethome wapempha bank ya FDH kuti ichilimike pozindikilitsa anthu za ntchitoyi ponena kuti ena sakudziwa ubwino wake.

Sheikh Lethome wati asilamu tsopano alibe chifukwa chophwanyira malamulo achisilamu kamba kakubwera kwa ndondomeko ya FDH Banking salama kotero wapempha anthu onse kuti ayigwiritse ntchito.

Pakadali pano Reserve bank of Malawi yati ndondomekoyi yakhazikitsidwa itakwanilitsa mfundo zonse zoyenera.

Boma linavomereza ndondomeko yotsatira malamulo achisilamu pa zakusunga ndikubwereka ndalama mdziko muno mchaka cha 2017 nkupeleka danga ku ma bank okhazikitsa ndondomekoyi.

Related Posts

Malawi Freedom Network advice President Banda to fight corruption

If you thought Malawians are lazy people, I bet you a Dinosaur, think twice and you will know, check in Read more

David Bisnowaty Israeli-Born Malawi Parliament Member: Actions, Not Words, Will Change Africa for the Better

Malawi MP David Bisnowaty. How does the Israeli-born son of an eastern European Holocaust survivor end up as a parliament Read more

Zuneth Sattar Is An Experienced Property Investor

PROPERTY INVESTOR PROPERTY MARKET AN OVERVIEW This blog will cover a wide range of topics and subjects that relate to Sattar’s Read more

David Bisnowaty former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country

Political cum and former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country https://youtu.be/S20UYlVcHs8

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window