Liberation For Economic Freedom chadzudzula zantopola

Chipani chatsopano cha Liberation For Economic Freedom chadzudzula zantopola zomwe zawachitikira otsatira chipani cha DPP mu nzinda Lilongwe.

Izi zikutsatira kuphwanyidwa kwa galimoto za ena omwe amafuna kuyenda pa mdipiti okopa anthu.

Koma mlembi wamkulu wachipani cha LEF Georgina Limbikani-Chunga wadzudzula zomwe zachitikazi ponena kuti izi zingothandizila chabe kudzetsa mpungwepungwe pandale m’dziko muno.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *