Oletsetsa ndewu savula shati–Chilima

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima wafika mu nzinda wa Mzuzu madzulo ano pomwe mawa Lamulungu akuyenera kukhala nawo pa mwambo okumbukira a malitili omwe uchitikire m’boma la Nkhata Bay.

Anthu ochuluka anasonkhana pa Roundabout ya Shoprite kudikira a Chilima kuti awayankhule.

Koma iwo anayamika anthuwa powadikira ndipo anamaliza ndi mwambi omwe oti: ‘Oletsetsa ndewu savula shati’

Ena mwa omwe anawalandira a Chilima ndi nduna ya zokopa alendo a Vera Kamtukule ndi atsogoleri ena a chipani cha UTM mchigawo chakumpoto komanso mfumu ya nzinda wa Mzuzu a Gift Desire Nyirenda.

Dr Chilima

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *