Mon. Apr 29th, 2024

Sitinatseke Zipata Za Pa Liwonde Barrage

Tikudutsitsa madzi oposera mulingo wa 800,000 litres pa second

Akuluakulu a boma atsindika kuti saanatseke zipata zothandiza kudutsitsa mulingo woyenera wa madzi mu mtsinje wa Shire pa Liwonde Barrage.

Iwo anena izi Lachisanu (12th April, 2024) pa zokambirana ndi akuluakulu omilira okhudzidwa ndi kukwera kwa mulingo wa madzi m’boma la Mangochi.

Izi zalankhulidwa pomwe pakhala pakumveka kuti kusefukira kwa madzi m’boma la Mangochi kwadza chifukwa cha kutsekedwa kwa zipata za pa Liwonde, zomwe aakuluakulu a boma ananena mobwereza kuti sizinachitike.

Pa zokambiranazo, zomwe zinatsogoleredwa ndi Mlembi Wamkulu ku Nthambi Yoona Za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi a Charles Kalemba, Mlembi Wamkulu ku Unduna Woona za Madzi a Elias Chimulambe anati padakali pano, zipata za pa Liwonde zikudutsitsa madzi okwanira 957,000 litres pa second omwe ndi oposa mulingo wofunikira wa 800,000 litres pa second ndipo kukwera kwa mulingo wa madzi mu Nyanja ya Malawi komanso Shire kwadza chifukwa cha kugwa kwa mvula yambiri m’dziko la Tanzania komanso m’madera a kumpoto kwa dziko lino.

Iwo anati kutsegula zipata zonse 14 za pa barrage’yi kutha kudutsitsa madzi wokwana 4.2 million litres pa second zomwe zingapangitse kusefukira kwa madzi kosasimbika m’madera a chigwa cha mtsinje wa Shire komanso kusokonezeratu kapangidwe ka mphamvu za magetsi m’dziko muno.

M’mawu awo, a Kalemba anapempha akuluakulu oimira okhudzidwa kuti akafotokozere anthu tchutchutchu wa zomwe aona pa Barrage’yi komanso zomwe zadzetsa kusefukira kwa madzi m’madera mwawo.

“Tipiriza kuunika za momwe tingathetsere vutoli kwa nthawi yaitali komanso tibwera kudzakumana ndi okhudzidwa m’masiku akudzawa. Panopa, takonza kale zopititsa chimanga komanso ma tent kwa okhudzidwa omwe akusowa pokhala ndipo ndikutsimikizireni pano kuti tipititsanso lipoti la zokambirana zathu kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ,” anatero a Kalemba.

Mmodzi woimira anthu okhudzidwa Khansala Wellington Mangulenje anathokoza boma pokonza zokambiranazi koma anapempha kuti pakhale ndondomeko zokhazikika zothetseratu vutoli.

Pa zokambiranazi, zomwe zinayambira m’kachipinda komata mpaka pa zipata za pa Liwonde Barrage, panalinso Alembi Aakulu owona za Malo komanso Chilengedwe, akuluakulu a Nthambi ya National Water Resources Authority, makhansala, phungu wa Nyumba ya Malamulo, abwanamkubwa ndi mafumu.

Related Posts

The British NCA Operations In Malawi Remain Questionable, Britons Aim To Topple Tonse Government

Exposed! British NCA bankrolls PIJ to victimize successful business persons, politicians, judges in Malawi The truth be told! The establishment Read more

Mirece supports land reclamation bought by foreigners

Reverend Flywell Somanje…. this is the way to go A governance and human rights organization, the Millennium Information and Resource Read more

NBM Donates K100 Million Towards Forest Restoration

National Bank of Malawi has committed K100 million for preservation and restoration of 6 natural resources in the country by Read more

I am not a crook— Mulli

MAINTAINED THAT PROCEDURES WERE FOLLOWED—Mulli— Picture by Catherine Maulidi Businessperson and National Bus Services Chairperson Leston Mulli on Tuesday told Read more

Other stories

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Ekhaya luxury Resort fully open