Chigamulo Cha Kamwendo Sichinayende Bwino
Pamene kwangotsala masiku atatu, kuti osewera wa Premier Bet Dedza Dynamos, Promise, akwanilitse masiku omwe akuyenera kubweza K6 million ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers kamba kolephereka kwa transfer yake, Football Players Association (FPA) yadzudzula kuti chigamulo cha osewerayu sichinayende bwino.
Kamwendo anauzidwa kuti abweze ndalamayi transfer itakanika kamba koti inali ndi zolakwika zochuluka.
Mlembi wa FPA, Ernest Mangani, wati FAM ikuyenera kukonzanso malamulo awo okhuza nkhaniyi kamba koti akupyinja osewera.
Read also: Mlakho Wa Lhomwe Supports Govt To Save Money Hence Will Not Invite Chakwera
Read also: The Hidden Struggles Inside Malawi’s Public Hospitals
Read also: Charles Nsaku’s “Economy” Music Sparks Rallying Cry for APM Leadership
Mangani watinso pakhala povuta kuti osewerayu abweze ndalama zomwe analandira kamba koti amakhala agwiritsa ntchito zina.
Osewerayu anasaina kontirakiti ya zaka zitatu ku Lali Luban, zomwe zinapangitsa FCB Nyasa Big Bullets kukang’amala ku Football Association of Malawi (FAM) kuti osewerayu anali atamvana naye chili chonse kuti apite ku Maule.
Chigamulo chomwe komiti yoyang’anira osewera ku FAM inapereka, inagamula kuti Kamwendo abweze K6 million zomwe analandira ku Nyerere pasanadutse masiku 14, Dedza ibweze K3 million ku Bullets komanso K4 million ku Manoma kamba koti transfer sinavomerezedwe.
Read also: MCP accused of paying attendees to boost numbers at Ekwendeni Rally
Read also: Analysis of Lawyer Alexius Kamangila’s live broadcast on judicial corruption





