By Malawi Freedom Network (MFN) | 15 November 2026
Omvera a Radio Islam mdera la Kanengo Zone asonkhana mwaunyinji pamsonkhano womwe cholinga chake chinali kulimbikitsa mgwirizano, umodzi komanso chitukuko cha bungwe la Radio Islam Listeners mderali.
Pamsonkhanowu, womwe wachitika ku Kanengo Zone Headquarters pa Cleraz Mosque, Area 25, Kanengo, mamembala ochokera m’madera osiyanasiyana asonyeza chidwi chawo pothandizana kulimbikitsa ntchito za bungweli.
Polankhula pamsonkhanowu, Trustee wa Kanengo Zone komanso yemwe kale anali Purezidenti wa Radio Islam Listeners Association, Brother Suleman AtupeIe Chitera, watsindika kufunika kwa umodzi, mgwirizano ndi kudzipereka ngati njira zolimbikitsira bungweli.
Chitera wati mphamvu ya bungwe lililonse imachokera ku mgwirizano wa mamembala ake, ndipo sizingatheke kumanga bungwe lolimba ngati anthu ake ali ogawikana, osamvana kapena kugwira ntchito motsutsana.
Iye walimbikitsa mamembala ochokera ku Chatata Area, Mgona, Area 49, Chimoka, Chakhuta Madzi, Lumbadzi ndi madera ena kuti aziona kuti onse ali ndi udindo wofanana pa chitukuko cha Kanengo Zone.
“Radio Islam Listeners si ya munthu mmodzi, si ya atsogoleri okha, koma ndi ya tonsefe. Choncho, tsogolo lake lili m’manja mwathu tonse,” adatero Chitera.
Chitera watsindikanso kuti kukhala membala wa Radio Islam Listeners sikuyenera kungokhala ndi dzina m’kaundula kapena kungomvera wailesiyi, koma kuyenera kutsagana ndi kutenga nawo mbali pa zochitika za bungwe, kuthandizana komanso kulimbikitsa ena.
Iye walimbikitsanso atsogoleri kuti azikhala odzichepetsa, omvera maganizo a anthu komanso okonzeka kutumikira mamembala m’malo mongofuna maudindo.
Chitera wati akufuna kuona Kanengo Zone ikukhala chitsanzo chabwino kwa madera ena kudzera mu njira zabwino zogwirira ntchito, kulimbikitsa achinyamata komanso kukhazikitsa mgwirizano pakati pa atsogoleri ndi mamembala.
Pamsonkhanowu, Mayi Kaunga ayamika mamembala chifukwa chopezeka mwaunyinji komanso kusunga nthawi, ponena kuti kupezeka kwawo ndi chizindikiro cha chidwi chawo pa ntchito za bungweli.
Brother Haroon Duli nayenso wayamikira mamembala chifukwa cha msonkhano wabwino womwe wachitikawu, ndipo walimbikitsa aliyense kuti azidzipereka pogwira ntchito za bungwe kuti zolinga zake zitheke.
Kumbali yake, Brother Stanley Kapichira wayamikira Chitera chifukwa cha kudzichepetsa kwake komanso kulimbikitsa kuyambiranso kwa ntchito za Kanengo Zone ndi mtima wachimwemwe komanso mgwirizano.
Brother Kapichira walimbikitsa mamembala kuti ayambe ulendo watsopano wa chitukuko popanda kunyamula zakale zomwe zingasokoneze mgwirizano wawo.
Pamene Brother John Mambo wakumbutsa mamembala kuti msonkhano wotsatira ukuyembekezeka kuchitikira ku Chatata sabata yamawa, pofuna kupitiriza kulimbikitsa mgwirizano pakati pa omvera a Radio Islam.
Brother Yusuf Chitsulo, yemwe wati anapezeka pamsonkhanowu atamva chilengezo choti kukuchitika msonkhano, wayamikira mwayi womwe wapeza chifukwa waphunzira zinthu zingapo zomwe zingamuthandize kutenga nawo mbali pa ntchito za bungwe.
Chitsulo wayamikiranso Chitera chifukwa cha kudzichepetsa kwake komanso zomwe akuchita polimbikitsa ndi kudzutsa Kanengo Zone kuti igwire ntchito mwakhama.
Nayenso Mayi Bhima wasonyeza chisangalalo chake chifukwa cha kuchuluka kwa mamembala omwe anapezeka pamsonkhanowu, ponena kuti kupezeka kwawo mwaunyinji kwasonyeza mphamvu ndi chidwi cha Kanengo Zone.
Pamapeto pa msonkhanowu, mamembala alimbikitsidwa kupitiriza kugwira ntchito limodzi, kulemekezana, kuthandizana komanso kupewa mikangano yosafunika yomwe ingasokoneze ntchito za bungwe.
Msonkhanowu ukuoneka ngati gawo lofunika kwambiri polimbikitsanso mgwirizano wa omvera a Radio Islam ku Kanengo Zone, pomwe mamembala akuyang’ana tsogolo lomwe lili ndi umodzi, kudzipereka komanso chitukuko.
Umodzi, Mgwirizano ndi Chitukuko zikhalebe maziko a Radio Islam Listeners ku Kanengo Zone.


