Olemba brother Jumbe
Pamene MAM ikukonzekera chisankho chatsopano, ndondomeko yonse iyenera kutsatira mfundo za chilungamo mowopa Allah.
Choyamba, ndalama zokwana MK5 miliyoni zomwe zikufuna kulipiritsidwa munthu wofuna kuyimira udindo ziyenera kuchotsedwa.
MAM ndi bungwe lachipembedzo, osati chipani cha ndale. Utsogoleri uyenera kutseguka kwa Msilamu aliyense woyenerera, osayang’ana kuchuluka kwa ndalama zomwe ali nazo.
Kuyimira udindo uliwonse mu MAM kuyenera kukhala kwaulere.MAM Blasts MCP Government for Snubbing Eidul Adhuha
Chachiwiri, pofuna kulimbikitsa mgwirizano ndi kuyambitsa tsamba latsopano, Sheikh Idrissah Muhammad sayenera kuyimira udindo uliwonse pa chisankhochi.
Chachitatu, komiti yomwe ikukonzekera chisankhochi iyenera kusinthidwa ndi komiti yodziyimira payokha komanso yopanda tsankho.
Gulu lililonse lomwe likuchita nawo chisankho liyenera kukhala ndi oyimira ake mofanana kuti chisankho chikhale chowonekera poyera, chodalirika, komanso chovomerezeka ndi onse.
Pomaliza, khoti liyenera kufotokoza bwino chigamulo chake ndi kupereka malangizo omveka bwino pa momwe chisankho cha MAM chiyenera kuchitikira, kuti chilungamo chitsatidwe ndipo mikangano ipewedwe.
Cholinga chathu chisakhale kupambana kwa munthu m’modzi pa udindo wa u chairman, koma kuteteza chilungamo, mgwirizano, ndi ulemu wa Muslim association m’malawi muno.
Mtumiki wa Allah (saw) anati;Opinion: Malawi Police, a force of oppression, not protection
Anthu okondedwa kwambiri kwa Allah ndi amene amapindulitsa kwambiri anthu ena.
Tikupepha Allah atitsogolere tonse ku chilungamo, atigwirizanitse pa choonadi, ndipo apatse MAM utsogoleri woona mtima komanso wodalirika ndiowopa iye Allah mwini wake.
Read also: Mozambique president jets in
Read also: Islamic Benefit Trust Hands Over 13 Houses To Tropical Ana Affected
Read also: Van Carrying Goods Worth MK10 Million Catches Fire in Machinga

