
Wolemba: Racheal Julaye
Anthu osadziwika akuganizilidwa kuti aba m’modzi mwa akukuakulu a kampani ya Universal Industries Muhammad Kasman lachitatu mu mzinda wa Lilongwe.
Mneneri wa polisi ya Lilongwe Hastings Chigalu watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati Kasman yemwe ndi mzika ya Britain, wabedwa akuchokera ku mzikiti mu mzindawu.
”Pakadali pano tapeza iPhone ya a Kasman koma sititchula pomwe taipeza poti izi zitha kusokoneza kafukufuku,” watero Chigalu.
Iye wati Kasman amayendetsa galimoto la mtundu wa Toyota Fortuner CP 10842 ndipo anadabwa kuona kuti nsewu watsekedwa kutsogolo ndi anyamata omwe amaguza ngolo ndipo atatuluka kuti akaone ndi pomwe anthuwa anamugwira ndikumulowetsa m’galimoto yawo.
Chigalu wati pakadali pano kafukufuku Ali mkati kuti adziwe cholinga cha anthuwa komanso kupulumutsa bamboyu.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!