Olemba: Prince Hassan
Wochita malonda, Omar Ayatu, wa ku Chimwala m’boma la Mangochi, wathandiza gulu la azimayi achisilamu la Chimwala Dawa Group ndi ndalama zothandizira ulendo wawo wopita ku Ijitima ku Salima.
Thandizoli labwera potsatira pempho lomwe azimayiwa anapereka kwa Ayatu kuti awathandize kukwaniritsa cholinga chawo chopita ku Ijitima.
Poyankhula atapereka thandizoli, Ayatu adati aganiza zothandiza azimayiwa chifukwa cha kufunitsitsa kwawo kutenga nawo mbali pa mwambowu komanso kufunika kogawana zomwe munthu ali nazo ndi ena.
“Ndinaona kuti ndiwathandize azimayi amenewa ndi cholinga choti akwaniritse khumbo lawo lokakhala nawo ku Ijitima imeneyi. Sikuti ndine wolemera ayi, koma ndimakonda kuthandiza magulu a anthu ndikakhala ndi kuthekera.
“Anthu ambiri amaopa kuthandiza chifukwa choganiza kuti zomwe ali nazo zingathe, koma siziyenera kukhala choncho. Ngakhale zochepa zomwe tili nazo, tiyenera kugawana ndi ena potsatira chiphunzitso cha chipembedzo chathu cha Chisilamu.
“Kuthandiza sikutanthauza kukhala ndi zochuluka ayi, koma kumadalira mtima wa munthu. Ndikupemphani kuti zomwe mukaphunzire ku Ijitima imeneyi zidzakulimbikitseni kukhala Asilamu abwino,” adatero Ayatu.
Polandira thandizoli, m’malo mwa gulu la Chimwala Dawa Group, Sister Lubia Nkozombe anathokoza Ayatu chifukwa choyankha mwachangu pempho lawo ngakhale kuti anali ndi zosowa zambiri.
Nkozombe adati anthu ena akapemphedwa thandizo amakonda kufufuza zinthu zambiri, zomwe zimachititsa kuti thandizo lochedwa lifike kwa omwe akulifuna.
“Anthu ena akapemphedwa thandizo amafufuza zambiri, nthawi zina kufuna kudziwa ngati pali zandale, ndipo izi zimatenga nthawi. Koma inu titakupemphani, nthawi yomweyo munatiyankha.
“Ambuye akudalitseni pa ntchito zachifundo zomwe mukugwira, ndipo Allah akupatseni zabwino. Anthu ena akakhala ndi chuma amadzitukumula moti zimavuta kuwafikira, koma inuyo simuli choncho,” adatero Nkozombe.
Pakadali pano, Ayatu akuchita ntchito zosiyanasiyana zachifundo m’dera la Mangochi Nkungulu Constituency, kuphatikizapo kukonza mizigo yoonongeka, kupereka mayunifolomu kwa ana asukulu komanso kuthandiza kukonza msewu wa Mpale-Chapola.
Msewu wa Mpale-Chapola ndi wautali makilomita asanu ndi limodzi (6km), ndipo Ayatu akuti akuthandiza pa ntchito yokonza mseuwu pogwiritsa ntchito ndalama zake.
Thandizo lomwe wapereka kwa azimayi a Chimwala Dawa Group likuwonjezera pa ntchito zachifundo zomwe akuchita m’derali, makamaka pothandiza anthu kukwaniritsa zosowa zawo komanso kulimbikitsa mgwirizano pakati pa anthu.



