Mmodsi mwa akuluakulu achipani cha UTM a Dr Dalitso Kabambe wati chipani Cha UTM sichikupanga alliance ndi chipani china chilichonse. Iye wati Chaka Cha mawa chipanichi chizakhala pa ballot paper ndipo omwe akufuna alliance akonzeke kukhala pambuyo.
Dr Dalitso Kabambe Kabambe waonjezeratso kuti chuma sichikuyenda kamba kosowa utsogoleri. Iye wati pakadali pano dziko la Malawi likuyenda opanda oliyendetsa chifukwa anthu omwe anasankhidwa ngati atsogoleri atanganidwa ndikusakadza chuma cha boma.
A Kabambe ati anatuluka chipani Cha DPP kwamuyaya ndipo sazachilowatso. Dr Kabambe wati iye anasankha kukhala wa UTM chifukwa ndichipani chomwe sichikugawanitsa mitundu ya anthu.iye wadzuzula chipani Cha MCP komanso DPP pokhazikitsa ulamuliro wa sankho ndipo wati Amalawi ayembekezere Umodzi kuyambira 2025.
Read also: Dzamalala To Postmortem Bodies Found In Mass Graves
Read also: Government Releases K100 Billion to Boost Maize Stocks, Vows No Malawian Will Die of Hunger
Read also: Jane Ansah: A leader who understands Malawians’ everyday struggles

