Silver Strikers yalumira mano pa khumbo lake lofuna kutenga TNM Super League pamene yagonjetsa timu ya Mighty Tigers 2-0 pamasewero omwe analipo lero pa bwalo la Silver mu nzinda wa Lilongwe.
Friday Osagie anali katswiri odalirika pamene anamwetsa zigoli ziwiri yekha kupangitsa kuti Ma Central Bankers azitsogola ndi mapointi 43 pamasewero 17 omwe asewera.
Ndi m’mene zilirimu ndiye kuti anyamata a Pater Mponda atsegula danga la mapointi asanu ndi atatu kwa Mighty Mukuru Wanderers yomwe ili panambala yachiwiri ndi mapointi 35 pamasewero 18 omwe asewera.
Zotsatira za masewero ena omwe analipo lero zinali motere:
Moyale Barracks yagonjetsa Karonga United 1-0, chigoli chomwe anagoletsa ndi Emmanuel Allan pamasewero omwe analipo pa bwalo la Mzuzu, pamene Chitipa United yafanana mphamvu ndi Mafco FC osagoletsana chigoli chilichonse pamasewero omwe anachitikira pa bwalo la Karonga.
Read also: Chakwera defends foreign trips, appeals for international support
Read also: IZF Resumes Student Bursaries After Four-Year Hiatus
Read also: A call for change: Why Malawians must reject DPP and MCP in 2025

