Zipani zina zotsutsa boma m’dziko muno zati palibe cholepheretsa ziwonetsero zomwe akonza kuti zichitike tsiku la lero.
Izi zikudza ngakhale apolisi adati lero ali ndi ntchito zina zoti agwire kotero sapezekako ku ziwonetserozi.
Zokambirana pakati pa mbali ziwirizi zalephera kubwera ndi mfundo imodzi ndipo agwirizana kusagwirizana.
Zipanizi zomwe n’kuphatikizapo UDF, UTM, AFORD, DPP komanso EFP zati sizokhutira ndi kagwiritsidwe ntchito ka bungwe la MEC komanso NRB.
Kotero akuyembekezeka kuchititsa ziwonetsero ku Lilongwe zomwe akufuna kuti adindo ena ku MEC atule pansi maundindo awo komanso kusintha momwe ndondomeko ya kalembera wa zisankho ikuyendera.
Read also: MDF Takes on FISP Corruption in Makanjira, Demands Action from ACB and Agriculture Ministry
Read also: Chitsulo walks her last mile in Mwanza.

