Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers a Thom Mpinganjira wati ndi wokondwa ndi m’mene timuyi ikuchitira pa masewero ake a mu ligi ya TNM.
A Mpinganjira ati apempha osewera a timuyi kuti adzipereke kwatunthu pa masewero omwe atsala nawo kuti apitilire kupereka mpikisano wa ukulu ku timu ya Silver Strikers yomwe ikutsogola pakadali pano.
Iwo ayamikiranso osewera wa pakati wa timuyi Isaac Kaliati kaamba komwetsa zigoli zisanu ndi zitatu mu ligiyi.
Wanderers ndi yachiwiri pa ndandanda wa matimu mu ligiyi ndi ma point 34 pamasewero 18 pomwe Silver ikutsogola ndi ma point 40 pamasewero 16.
Wolemba Peter Fote
Team manager wa Wanderers Steve Madeira kusangalala ndi Kaliati.
Read also: Apolisi a Malawi akuimbidwa mlandu wokakamiza a Mussa kuti anene zabodza
Read also: Critical questions on violence against Civil Servants
Read also: 6th Wealth Creation Conference Kicks Off in Blantyre: “Innovate, Invest, Impact

