Bungwe la Coaches Association of Malawi yalangiza mamembala ake kuti adzikhala oleza mtima pomwe akugwira ntchito yawo kupewa kupanga ziganizo zolakwika.
Bungweli layankhula kutsatira kusowa kwa Meke Mwase, ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers chigonjereni ndi timu ya Silver Strikers mu mpikisano wa Airtel Top 8.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Davie Mpima, wati m’malo monyanyala aphunzitsiwa aphunzire kudalira pemphero kuti mulungu adziwathandiza kupanga ziganizo zoyenera.
”Ngati bungwe sitinamve kalikonse kumbali ya Meke Mwase koma nkhala pa mpando wathu Aubrey Nankhuni anayesa kufikira ku Wanderers komwe wayankhidwa kuti sakupezeka ndipo ma phone ake ndiozimitsa,” watero Mpima.
Kufikira tsiku la kusowa kwake, Mwase anali mphunzitsi wamkulu wa timuyi pomwe anatenga udindo kutsatira kusiya ntchito kwa yemwe anali mphunzitsi pa nthawiyo Nsanzurwimo Ramadhan.
Read also: Betrayal in Life, Silence in Death: The Unsettled Spirit of Malemu Kazombo
Read also: Desperation on the Highway: Women Collect Maize Spilled from Moving Truck as Hunger Bites Malawi
Read also: Kamphangala advises Muluzi’s family to leave Bakili Muluzi TV alone

