Chipani UTM chati chiwonetsetsa kuti mfundo za mgwirizanowu zatsatiridwa
Chimodzi mwa zipani zomwe zili mu mgwirizano wa Tonse, cha UTM chati chiwonetsetsa kuti mfundo za mgwirizanowu zatsatiridwa.
Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM wayankhula izi pomwe kwadutsa zaka zinayi chichokereni pomwe zipani za UTM komanso MCP, mwa zina, zinapanga mgwirizano wa Tonse.
Mgwirizanowu unapangidwa pa 19 March mchaka cha 2020.
Poyankhula ndi MIJ Online, Kaliati wati chipanichi chili ndi chidwi chofuna kuona ngati ma membala a mgwirizanowu akwanilitse mfundo zomwe anagwirizana m'mbuyomu.
"Mu zaka zinayi zapitazi, ife ngati chipani cha UTM taphunzirapo zambiri mu mgwirizanowu ndipo tili ndi chidwi pofuna kuona mathero a mgwirizanowu, "watero Kaliati.
MIJ Online, inayesera kuyankhula ndi Eisenhower Mkaka mlembi wamkulu wa chipani cha MCP yemwe anati tiyankhule ndi...